Psalms 112

1Tamandani Yehova.

Wodala munthu amene amaopa Yehova,
amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake.

2Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko;
mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa.
3Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake,
ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
4Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima;
wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima.
5Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu,
amene amachita ntchito yake mwachilungamo.

6Ndithu sadzagwedezeka;
munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya.
7Saopa akamva zoyipa zimene zachitika;
mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova.
8Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha;
potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano.
9Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka,
chilungamo chake chimanka mpaka muyaya;
nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu.

10Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima;
adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka.
Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.
Copyright information for NyaCCL